Chichewa Christian Hymns
Hymn 364 DZUŴA lapitira,
DZUŴA lapitira,
Wadza mdimawo,
Mthunzi wamadzulo
Wagwa m’mwambamo.
M’mwambamo nyenyezi
Zithwanima mbee;
Zonse zili m’tulo
Pansi pali duu.
Yesu mutipatse
Tulo toti phee;
Ndi mdalitso wanu
Mndigonetse ’ne
Mpatse ana ’ng’ono
Alotemo mbee;
Anthu aulendo
Msungesungebe.
Mutonthoze mtima
Wopwetekawo;
Akutsata tchimo
Mletse onsewo.
Wonsewu usiku
Andisunge ’ne
Amithenga anu
Akuyera mbee.
Ndidzukanso m’maŵa,
Kucha koti mbuu,
Ndiyeretu mtima
M’maso mwanumo.
Titamadi ’Tate,
Mwana wakeyo,
Mzimu Woyeranso,
Nthaŵinthaŵizo.
