Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 362 MUKHALE ndine, dzuŵalo laloŵa,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 362 MUKHALE ndine, dzuŵalo laloŵa,

 

MUKHALE ndine, dzuŵalo laloŵa,
Wagwa usiku, bwenzi lindisoŵa;
Ndilibe wina wakundithandiza,
Wamphamvu ndinu, mkhale ndinetu.

Kamoyo kanga katha lero lino,
Zidzachokanso zinthuzo za dziko;
Zimasinthika zonse zooneka,
Simusi nthika, mkhale ndinutu.

Koma kalelo mnakhalitsa pano,
Mukhale ndine, msandichokerenso,
Sin’pempha kuti Mbuye mungotsotse,
Komatu mukhalitse ndinetu.

E, tsiku lonse Inu ndifunitsa;
Ndi mphamvu yanu yokha ndisungika;
Mukatsogola ndidzadikha m’mtima;
Usiku, msana, mkhale ndinetu.

Adani sindiopa mukalipo
Muletse tsoka ndi chisoni chino;
Ikadza imfa n’dzalimbika m’mtima;
M’moyo ndi m’imfa mkhale ndinetu.

Exit mobile version