Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 339 MTIMA wanga ndikonzera,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 339 MTIMA wanga ndikonzera,

 

MTIMA wanga ndikonzera,
Mbuye Yesu aitana;
Ati: “Mwana, tapemphera,
Ine sindidzakukana.”

Mbuye ndinu Mfumu yanga
Yolemera ndi yamphamvu;
Ndikapemphatu zambiri,
Simundimanira kanthu.

Ndikabwera nd katundu
Wa zoipa zanga zonse;
Mwazi wake wa Ambuye,
Udzandiyeretsa konse.

Mbuye ndinalema ine,
Mloŵe Inu m’mtima mwanga;
Mkhale m’mwemo mwini wake,
Mantha mwandichotsera ’ne.

Ndine mlendo pansi pano,
Mndilimbitse ndi chikondi;
Bwenzi mundilondolere
Njira pa ulendo wonse.

Mndidziŵitse ntchito yanga,
Mphamvu yake mundipatse;
Mundilimbikitse m’mtima
Ndikhale kwa Atate.

Exit mobile version