Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 338 ’TATE wa Kumwambako,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 338 ’TATE wa Kumwambako,

 

’TATE wa Kumwambako,
Likayere Dzinalo,
Udzetu Ufumu wanu;
Chifuniro chanucho
Chichitike pansipa
Monga chachitika kwanu.

Mutipatse leroli
E, chakudya chathuchi
Tsiku n’tsiku tichilira.
Mukhululukiredi
Tchimo lathu, monga ’fe
Iwo adatichimwira.

Musatifikitsemo
Muli mayeserowo,
Koma mutipulumutse.
Wanu ndi ufumuwo,
Mphamvu ndi ulemunso
Kufikira nthaŵi zonse.

Exit mobile version