Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 336 KULINSO dziko lowala M’mwamba,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 336 KULINSO dziko lowala M’mwamba,

 

KULINSO dziko lowala M’mwamba,
Kunthawi zosatha;
Komwe kulibe mdima bii,
Yesu ndiye nyaliyo.

Mtandawo tidzasenza,
Korona tidzavala,
Pamodzi ndi oyera,
M’dziko la Kumwambako.

Chikondi chake cha Mlengi wathu,
Natuma Yesuyo;
Kudzatifera tonsefe,
Ndikutipatsa moyo.

Mulitu ulemelero M’mwamba,
Kwa anthu omvera;
Omwe akonda Yesuyo,
Ndikugwira ntchitoyo.

Exit mobile version