Chichewa Christian Hymns
Hymn 320 NDIKONDA Mlungu pomva Mbuye wanga
NDIKONDA Mlungu pomva Mbuye wanga
Amva pemphero ndi kulira kwanga,
Namachereza khutu nditapfuula,
Andithandiza, nandipulumutsa.
Mulungu wanga ndiye wachifundo
Ndi wolungama mtima ndi wabwino;
Apulumutsa anthu akufoka,
Akathandiza nkhaŵa imachoka.
Mtimanga, bwera kuti upumule,
Wakuchitiranso zokoma Mbuye,
Wakuchotsera imfa ndi misozi,
Ndingakhumudwe asungira phazi.
Nditani ine kubwezera Mbuye
Zokoma zonse anandichitira?
Chipulumutso chake ndidzatama,
Ndinalumbira zija ndidzapatsa.
Imfa ya anthu ake imkomera,
Aŵalandira m’nyumba zokonzeka.
Mbuye, kapolo wanu ndipereka
Nsembeyi yonga yanu, ndine ndekha.
