Chichewa Christian Hymns
Hymn 309 ANA akumwamba ndife,
ANA akumwamba ndife,
Paulendo timaimba;
Timatama Mbuye wathu
Wa ulemerero wonse.
Tilikupita kwathu kuja
Munjira ya atate athu,
Amakondwera lero lomwe;
Tinka kuonana nawo.
Mbuye anatiitana
Kukagwira ntchito yake,
Kuitana anthu onse
Atsatenso njira yino.
Inde Mbuye, tibweradi,
Zathu zonse tizisiya,
Mtsogoleri wathu ndinu
Titsatabe inu nokha.
