Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 305 NDALIMVA dziko la m’talimo,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 305 NDALIMVA dziko la m’talimo,

 

NDALIMVA dziko la m’talimo,
Munthu sangathe kulisimba;
Malowo awala koposa,
Ndi Yesu tidzakhala naye.

Komweko, komweko,
Ndi Yesu tidzakhala naye.

Musazengereze anthuni,
Chimwemwe uko chilipodi;
Anthuni, mudzalandiradi,
Ndi Yesu mudzakhala naye.

Mwana’we pereka mtima’ko,
Akuchotsere zoipazo;
Udzakhala wokondweradi,
E! n’kwabwino lola mwana ‘we.

Idzani, mverani, lapani,
Chipulumutso chilipodi;
Kwa Yesu yemwe wofera ‘nu,
Ndi Yesu mudzanka
Kumwamba.

Exit mobile version