Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 302 NDIDZE pafupi pa

Chichewa Christian Hymns

Hymn 302 NDIDZE pafupi pa

 

NDIDZE pafupi pa
Mlungu wanga,
Ngakhale pamtanda
Mundikweza;
Koma ndiimbabe
Mbuye mndikhalitse,
Mbuye mndikhalitse,
M’fupi Ndinu.

Ngakhale kuthengo
Ndasokera,
M’mdima ndigonapa
E, pamwala;
Koma m’kulotako
Ndiyandikizanso,
Ndiyandikizanso
M’fupi Ndinu.

Pajapo ndipenya
Pokwerapo,
Angelo atsika
Kumwambako,
Ndiwo akodola
Kuti ndikabwere,
Kuti ndikabwere
M’fupi Ndinu.

Tsopano poukanso
Wokondwatu,
Ndipeza pomwepo
Pali Mlungu;
Ndipo masautso
Andisendezanso,
Andisendezanso,
M’fupi Ndinu.

Pena pakufadi,
N’kwera m’Mwamba,
Dzuŵa ndi nyenyezi
Zitsalira;
Pomwe ndiimbanso,
Ndidza pafupi pa,
Ndidza pafupi pa
Mlungu wanga.

Exit mobile version