Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 300 AKRISTU limbikani,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 300 AKRISTU limbikani,

 

AKRISTU limbikani,
Imani mtima nji!
Mbendera nyamulani,
Msatenthemere ’yi.
Wotsogolera wathu
Ndi Mwana wa Mulungu;
Adzagonjetsa onse
Adani athuwo.

Tigwire nkhondo yomwe
Ya Mbuye wathuyo;
Tileke zakuipa
Zokhala m’mtimamo.
Sitikwanira tokha
Kuleka zathu zomwe,
Koma Mbuyathu Yesu
Atithangatatu.

Tsopano timenyana
Ndi zakuipazi;
Pamene nkhondo yatha
Tidzanka kwathuko.
Yesu adzalandira
Ankhondo ake onse;
Adzakhalika naye
Kumwamba komweko.

Exit mobile version