Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 294 POYESEDWA ine

Chichewa Christian Hymns

Hymn 294 POYESEDWA ine

 

POYESEDWA ine
Yesu mudzetu,
Mundipempherere
Ndisachimwetu.
Mukaona kuti
Ndilefukatu,
Mbuye mndilimbitse
Nazo mphamvutu.

Ndi zapansi pano
Ndikokedwadi,
Koma ndi chisoni
Mndiphunzitsedi;
Ndisaiŵalire
Za Getsemane,
Pena mtanda wanu
Yesu Mbuye ’Nu.

Mukandipweteka,
Ndipirirapo:
Nsembe yanga ndiyo,
Landirani ’yo.
Ndikachita mantha Sindithaŵa ’yi:
Mtima udzalimba,
Ndidzaima nji!

Pakumalizidwa
Moyo wangawu,
Pomwalira ine,
Mudze Mbuyetu.
Ndidzadzipereka
M’manja mwanumo:
Mpulumutsi Yesu
Mndilandireko.

Exit mobile version