Chichewa Christian Hymns
Hymn 287 POKONDWA ndi poona vuto
POKONDWA ndi poona vuto
Ndi tsoka pena mwayi,
Ndikumbukira, ndiimbira
Mulungu wangayo.
Kwezani nane Ambuyathu,
Timlemekeze yekha;
Popsinja mtima ndinamtchula,
Nandithangata ’ne
Angelo amazinga nyumba
Za anthu olungama;
Mulungu ateteza omwe
Amkhulupirira.
Laŵani chikondano chake;
Mudzadziŵitsa msanga
Kudala kwawo kwa anake
Omkonda Mbuyeyo.
Opani iye, nimuleke
Kuopa kanthu kena;
Mumtumikire mokondwera,
Akusungani ’nu.
Mulungu wathu Mmodzi yekha
Atate, Mwana, Mzimu,
Akhale ndi ulemerero
Wachikhalirewo!
