Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 285 DZIKO lino lapansi,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 285 DZIKO lino lapansi,

 

DZIKO lino lapansi,
Moyo ndi wovuta;
Nthawi zina kuseka,
Nthawi zina kulira;
Komatu Ambuye wathu,
Amatisamalira;
Mbale wanga pilira.

Pilira, pilira, mbale wanga pilira,
Dziko lino ndi lovuta
Mbale wanga pilira;
Linadana naye Mwana wa Mulungu,
Mbale wanga pilira.

Zabwino zimabwera,
Ndipo zimapita;
Dziwa kuti Ambuye,
Afunitsa iwedi;
Kuti ugwiretu ntchito,
Yakeyi m’dziko lino;
Mbale wanga pilira.

Tsikulo lilinkudza,
Lomwe Mbuye Yesu;
Adzanena kwa iwe,
Bwera upumuletu;
Kuzovuta ndi zowawa,
Zam’dziko lapansili;
Mbale wanga pilira.

Exit mobile version