Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 282 INU muli mehere,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 282 INU muli mehere,

 

INU muli mehere,
Wa dziko lapansi;
Ukasukuluka,
Sungakolerenso,

Yang’anani bwino,
Muyende m’njirayo;
Kuti mungagwetu,
M’zovuta za dziko.

Pamenepo sungakwanirenso kanthu,
Koma kuti ukaponyedwetu kunja.

Ndinu kuunika,
Kwa dziko lapansi;
Mudzi wapaphiri
Sungabisiketu.

Sungayatse nyali,
N’kuyivundikira;
Koma uyika pachoikapo chake.

Ndipo iwunikira onse
m’nyumbamo;
Chomwecho inu
muunikire dziko.

Kuti pakuwona,
Ntchitozo zabwino;
Alemekezedwe,
Mlungu ‘Tate wanu.

Exit mobile version