Chichewa Christian Hymns
Hymn 273 USAFUNE chuma chokha,
USAFUNE chuma chokha,
Pena masewero okha;
Koma za Mulungu zokha,
Zipambana zinazo.
Ukafuna kulemera,
Pempha chuma chosathera;
Ndiwo mtima wakuyera,
Ndi wokonda Yesuyo.
Zosawutsa uvomere,
Ndipo Yesu chaulere;
Chikondano ndi mtendere,
Alowetsa m’mtimamo.
Zonse umazinyadira,
Udzaleka kusilira;
Uli nazo zokwanira,
Pakupeza Yesuyo.
Mbiri yake ubukitse,
Anthu onse nuphunzitse;
Kwa Mulungu nufikitse,
Osokera onsewo.
Yesu sakusiya konse,
Mphamvu, nzeru, chuma chonse;
Akupatsa nsiku zonse,
Tsata Yesu yekhayo.
