Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 264 KHALATU woyera, pempheratu m’tseri;

Chichewa Christian Hymns

Hymn 264 KHALATU woyera, pempheratu m’tseri;

 

KHALATU woyera, pempheratu m’tseri;
Werengani Mawu masiku onsewo.
Uthenga omwe ali akufoka,
Madalitso ake ufunefunebe.

Khalani woyera, dziko laipadi;
Pemphera kolimba kwa Yesu
Mbuyathu.
Yang’anitsa Yesu ndi kumutsatira,
Kuti anthu ena aonenso Iye.

Khalatu woyera, akutsogozetu;
Usamtsogolere munjira zakozo.
Pokondwa ndi m’nsoni tsata Ambuyako
Khulupira Yesu ndi Mawu akewo.

Khalatu woyera, khalatu wofatsa;
Alilamulire ganizo lakolo.
Utatsogozedwa ndi Mzimu wakeyo,
Msanga udzagwira m’Mwamba ntchito yake.

Exit mobile version