Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 261 M’NDIYANDIKITSE nanu Yesu,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 261 M’NDIYANDIKITSE nanu Yesu,

 

M’NDIYANDIKITSE nanu Yesu,
Ndiyenderane nanu;
E, nditsamire pa ‘nu Yesu,
Panjira yonseyi.

Ndiwonetsere kuunika,
Kokoma kwanu Yesu!
Yabwino mbiri ndibukitse,
Yokondweretsayo.

Chitsime chakuyera ine,
Ndifananetu nacho;
Mundigwiritse ntchito zanu,
E, zanu zokhazo.

Mulamulire mtima, Yesu,
Ndi chifuniro changa;
Mulowe mwanga ngati Mfumu;
Kuti ndimvere ‘Nu.

Ndimamva njala kuno, Yesu,
Yakufunitsa Inu;
Kumwamba kwanu ndikukhumba.
Kukondwa nanuko.

Exit mobile version