Chichewa Christian Hymns
Hymn 258 MWA ine, moyo wanga ndi Yesu
MWA ine, moyo wanga ndi Yesu
(Yesu) Yemwe anafera ine,
Ndiye anandiwombola;
Yesu, Yesu.
Mwazi wake ndi chitsime changa,
(Yesu) Pamene ndikasambamo
Zochimwa zanga zidzatha;
Yesu, Yesu.
Yesu Mfumu, ine ndingadzafe
(Yesu) ngati mundisiya ndekha,
Kukhala ndekha sinditha;
Yesu, Yesu.
Yesu Mfumu, ine ndisekere
(Yesu) Inu Mpulumutsi wanga
Pamene mukhala nane;
Yesu, Yesu.
