Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 256 NGATI mtima sumakonda

Chichewa Christian Hymns

Hymn 256 NGATI mtima sumakonda

 

NGATI mtima sumakonda
Yesu supumula bwino;
Mbuye, suwu mtima wanga,
Ndiwo wanu, mulandire.

Dziko lonse ndilitaya;
Ndikondetsa Yesu Mbuye;
An’komera kopambana
Andikondweretsa ndiye.

Ndakudani, mnandikonda
Ndi kukhetsa mwazi wanu.
Simuleka kundikonda;
Ine sindidzalekanso.

Mndisungire mtima wanga,
Uzikhulupira Inu,
Kuti moyo wanga wonse
Ubisaletu mwa Yesu.

Exit mobile version