Chichewa Christian Hymns
Hymn 255 KHALA chete mtima wanga
KHALA chete mtima wanga
Mlungu wako ndiye Mfumu;
Zinthu zonse zisinthika,
Mlungu ndi wachikhalire.
(Khala chete, Chidzakupinga n’chiyani?
Usaope, Mulungu ali nawe.)
Anthu onse pansi pano
Sakhutitsa mtima wawo;
Amadera zinthu zawo,
Namakhumba zakutali.
Khala chete mtima wanga,
Zikwanire zinthu zako;
Usakhumbe zapansipa
Koma Mlungu wako yekha.
