Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 249 MBUYANGA Yesu, mundigwire

Chichewa Christian Hymns

Hymn 249 MBUYANGA Yesu, mundigwire

 

MBUYANGA Yesu, mundigwire
Dzanja.
Kuyenda ndekha sindikwana ’yi;
Mukandigwira dzanja langa, Mbuye
Sindikaopa kanthu kena ’yi.

Mbuyanga Yesu, mundisunge ine
Pafupi ndi ’Nu nthaŵi yonseyo;
Ndikasoŵatu Inu, Mpulumutsi,
Ndingosekera m’talimo.

Mbuyanga Yesu, ndikapanda Inu
Ukadza mdima m’mtima mwangamu;
Koma ndinutu dzuŵa langa ndithu
Lakuwalitsa m’mtima momwemu.

Mbuyanga Yesu, mundigwire dzanja
Pamene ine ndimwalirapo.
Mkhaletu m’fupi nthaŵi yomwe Mbuye,
Mundiloŵetse ine m’Mwambamo.

Exit mobile version