Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 247 MULUNGU anditsogolera,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 247 MULUNGU anditsogolera,

 

MULUNGU anditsogolera,
Ndapumula m’mtimamo;
Ayang’anira njira zanga
Nsiku zanga zonsezo.

Mulungu anditsogolera
Nsiku zanga zonsezo;
Ndidzatsatira Mbuye wanga
M’njira mwake momwemo.

Masiku ena pali mdima,
Ndivutidwa m’mtimamo;
Masiku ena ndikondwera
Ndi zabwino zangazo.

Masiku onse m’mtima mwanga
Ndili ndi mtenderewo,
Chifukwa ndimakhulupira
Mtsogoleri wangayo.

Exit mobile version