Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 239 TILI ndi mtendere

Chichewa Christian Hymns

Hymn 239 TILI ndi mtendere

 

TILI ndi mtendere
Wopambanatu,
Monga ngati mtsinje
Mumitimamo;
Koma mtsinje uno
Umayenda phee,
Nthaŵi zonse mtima
Nutonthozabe.

Tikakhulupira
Mlungu wathuyo,
Tidzaona mwayi
Ndi mtenderewo.

Dzanja la Mulungu
Litisunga nji!
Nkhondo ya Satana
Sitiopa ’yi.
Zaphokoso zonse
Ndi zoopsyazo
Sizibvuta mtima,
Siziloŵamo.

Masauko athu
Ndi zokondwazo,
Azilola zonse
Ndi Atatewo.
Pokhulupirira
Tidzapezabe
Kuti mtima wake
Utikonda ’fe.

YESU ndiye Mbuye wanga,
Ndamva Mawu akewo
Andilandira ine,
Nandipulumutsatu.
Mwalembedwa mukalata
Mawu ake omwewo,
Kuti iwo akumvera
Akalandiridwatu.

Ndinakahala wakuipa, Ndinamkana kalelo;
Koma Yesu waiŵala
Mphulupulu zangazo.

Wapumitsa mtima wanga,
Kaamba ndaphunziratu
Mau ake olembedwa
Mukalata mwakemo.

Mumvetu abwenzi athu,
Musakanirire ’yi;
Yesu aitana inu,
Zalembedwa zomwezi.

Exit mobile version