Chichewa Christian Hymns
Hymn 238 MULUNGU wanga,
MULUNGU wanga,
Ndapeza moyo;
Ndili wokondwera
Masiku onse.
Aleluya, muyenera!
Aleluya, Amen.
Aleluya, ndidzamtama
Mulungu wanga.
Mwazi wa Yesu
Unditsukatu,
Ndiye Mbuye wanga
Ndi Mpulumutsi.
Pamtanda wake ’Nafera ine,
Ndi zoipa zanga ’Nazichotsadi.
Mulungu wanga
Andilandira,
Chifukwa cha Yesu
Mwana wakeyo.
Adzabweranso
Kundilandira
Ndikhale ndi Iye
Masiku onse.
