Chichewa Christian Hymns
Hymn 231 AMBUYE, m’imfamo
AMBUYE, m’imfamo
Munandikonda ine;
Sindikaniza ’Nu
Kanthu konse ’yi.
Ndimagwadira ’nu.
Ndikonda m’mtimamu,
Ndidzaperekatu
Nsembe yangayi.
Kumwamba kwanuko
Mundipempherere;
Ndikhulupirako,
N’dzalandiradi;
Ndisenze mtandawo,
Ndikhale mboniyo,
Ndiperekeko
Mitoloyi.
Ndikhumba mtimawo
Wofatsa ndithu,
Kuti ndiyambe ’ne
Ntchito zanuzi;
Akusokerawo,
Abwere kwawoko,
Inde,kwanutu.
Zambiri zangazo
Mnandipatsa kale,
Ndibweza zonsezi
Kwa Mbuyanga ’Nu;
Ndikadzaona ’Nu,
Mbuye wabwinotu,
Nsembe yokomatu
Ndidzakhalabe
