Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 222 NDILIKUMVA m’mtima mwanga

Chichewa Christian Hymns

Hymn 222 NDILIKUMVA m’mtima mwanga

 

NDILIKUMVA m’mtima mwanga
Mau ake a MbuyAnga,
Ati, “Ndakukonda iwe,
Kodi undikonda Ine?”

Ati; “Mwana, kumbukira
Zonse ndinakuchitira;
Ndakukonda, ndakufera,
Ndakufuna posokera.

“Ku zoipa zonse zako,
Goli la pakhosi pako,
Ndi kunthenda zosautsa
Ndine ndakupulumutsa

“Kodi mayi wobereka
Mwana wake adzamleka
Pena adzamwiŵalira,
Koma ndikukumbukira.

“Nthaŵi ilikudza yonse
Sindisinthanika konse;
Imfa sindiletsa Ine
Ndisakondekonde iwe.

“Ine ndidzakuonetsa
Zonse zakukondweretsa
Za Kumwamba zanga izo,
Mwana, sundikonda ine?”

Ambuyanga, ndalephera,
Mwachisoni ndipemphera
Mundipatse ine ndithu
Mtima wakukonda Inu.

Exit mobile version