Chichewa Christian Hymns
Hymn 213 INE ndili ndi manyazi
INE ndili ndi manyazi
Kuti kale lomwelo
Ndinanyoza kudza komwe
Kwa Mtetezi wanga Yesu,
Ndati, Sindimfuna `yi.
Koma Iye wandipeza;
Ndamuona m`mtandamo,
Mwa kufera ine momwe;
Ndipo ndati m`mtima mwanga:
Mbuye, ndikufunani.
Nsiku zonse kwanja kwake
Kunandithandizatu,
Kunandichiritsa mtima;
Ndipo ndati: Mpulumutsi,
Ndinu Mbuye wangatu.
Sindifuna Mbuye wina,
Koma Yesu yekhayo;
Ine ndili munthu wake,
Iye anandigonjetsa
Ndi kukonda kwakeko.
