Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 212 NDI MISOZI, ndi chisoni,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 212 NDI MISOZI, ndi chisoni,

 

NDI MISOZI, ndi chisoni,
Ndiliratu kwa Inu Yesu;
Ndi chifundo chandigwira,
Ndilira kutí ndili wanu

E! Kwa Inu, E! Kwa Inu!
Ndilira kuti ndili wanu.

Mbuye Yesu ndi Atate,
Mundiwona ndili wosowa;
Ndimasowa Mzimu wanu,
Kuinga zonse za mumtima.

Mtenderewo, wosanyenga,
Ndilira ine m’mtima mwanga;
Kundimvetsa chimwemwetu,
Ndilira ine m’mtima mwanga.

Kalekale ndinathawa,
Ndinakana kumvera Inu;
Koma lero ndamva kuti,
Muli mwini wake wa moyo.

Exit mobile version