Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 194 AMBUYE’naitan’ne;

Chichewa Christian Hymns

Hymn 194 AMBUYE’naitan’ne;

 

AMBUYE’naitan’ne;
“Dzapumulire kuno,
Tsamira mutu, mwana’we
M’chifuwa mwanga muno.”

Ndabwera kwa Ambuyeyo;
Wolema, wachisoni;
Anandipulumutsako,
Nakondweretsa ine.

Ambuye naitana’ne;
“Ndipatsa anthu madzi,
Wotopa ndi waludzu’we
Dzamwere moyo kuno.”

Ndabwera kwa Ambuyeyo.
Ndamwera madzi awa;
Laleka ndithu ludzulo,
Tsopano moyo wadza

Ambuye naitana’ne;
“La dziko ndine Dzuŵa,
Yang’ana Ine, kwacha’we,
Wachoka mdima uja.”

Ndayang’anira Mbuyeyo
Ndzapeza Dzuŵa langa
Londiyendetsa bwinoli
Pa njira yanga yonse.

Exit mobile version