Chichewa Christian Hymns
Hymn 184 LEKANI kubvutika ndi zinthu za padziko,
LEKANI kubvutika ndi zinthu za padziko,
Musekerere kuti tidzaimbira Yesu.
Imbira!
Timwimbire Yesu,
Mpulumutsi wathu!
Imbira!
Timwimbire Yesu,
Tonse tidzakondwera.
Musadziunjikire chuma cha padziko
Dzimbiri ndi njenjete
zimachiononga.
Koma mudziunjikire chuma cha Kumwamba
Kumene anapita Mtsogoleri wanu.
Aliponso adani am’kati ndi akunja;
Yesu watisekera, tidzakuimbirani.
Aliponse mabvuto, ena ndi oipa;
Yesu mutimasule kwa adani athu.
