Chichewa Christian Hymns
Hymn 181 PANALITU wakudwala
PANALITU wakudwala
Amene akakhala
Pakhomo la sunagoge:
Kuti anthu ena
Amuone iye.
Yenda iwe, yenda.
Yenda iwe, yenda,
Siliva ndilibe;
Mwa Yesuyo, yenda!
Kukondwa kwa wodwalayo
Kunali kopambana;
Iye anatumphatumpha,
Kuzungulira
Sunagoge yense.
Lero lino Mbuye Yesu
Aitana nonsenu;
Mukamvera ndi kumtsata,
Mudzakondwera
Ndi mdalitso wake.
