Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 178 ZAMBIRI zogona m’kholamo,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 178 ZAMBIRI zogona m’kholamo,

 

ZAMBIRI zogona m’kholamo,
Zosungika bwino ’mo;
Koma imodzi inasokeradi,
Nitayika m’thengomo
Kutali kuphiri loopsalo,
Kutali ndi mbusa wakeyo.

Ambuye, muli nazo zambirizi,
Kodi sizifikirazi?
Koma Mbusa nanena, “Yangayo
Yatayika naneyo;
Ngakhale njira njoopsadi,
Ndilinga kuphiri kuipezanso.”

Koma zina sizinadziŵa ayi,
Makwaŵa ’napyola ’Ye,
Ndi mdima woopsa wa usikuwo
Ambuye nailonda yake.
Anamva kulira kutaliko,
Naipeza yofoka, yakufayo.

Ambuye, wakuti ndi mwaziwo
Panjira ponsepo?
“Ndaukhetsa potsata iwetu,
Kukubweza ku kholalo.”
Ndi m’manja mwalaswa bwanjimo?
“Ndalaswa ndi minga pofuna iwe.”

Ndi ponse paphiri ndi padambopo
Ndi makwaŵa, indetu,
Kunakwera kupfuula Kumwambako,
“Kondwani, ndaipeza yanga!”
Nd’ angelo a Mlungu nabwezanso,
“Kondwani, Ambuye ’napeza yawo.”

Exit mobile version