Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 162 PENYETSETSA Yesu,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 162 PENYETSETSA Yesu,

 

PENYETSETSA Yesu,
Mtima wosauka; Anafera iwe,
Idza, nupumule.
Iye anachotsa
Nsoni ndi zoipa;
Penyetsetsa Yesu,
Ndi kukhulupira.

Penyetsetsa Yesu
Likatentha dzuŵa;
Yachuluka ntchito,
Mphamvu idzakula.
Akonzera kwawo
Nyumba zokhalamo;
Penyetsetsa Yesu,
Mtsatetu tsopano.

Penyetsetsa Yesu
Pogwirana nawo;
Nkhondo ikabvuta
Tamva Mbuye wako.
Achuluka’dani,
Iwe ungofoka;
Penyetsetsa Yesu,
Mantha adzachoka.

Ndipo pakuloŵa
M’dziko la Kumwamba,
Udzapeza komwe
Onse adzatama.
Mwa zoŵala zija
Za Kumwamba kwawo,
Udzapenya maso
Yesu Mbuye wako.

Exit mobile version