Chichewa Christian Hymns
Hymn 161 LERO lino mbale wanga,
LERO lino mbale wanga,
Ndilo tsiku lakukoma;
Talandira Mpulumutsi,
Mmene ali kuyitana.
Lero lino mbale wanga,
Usazengereze ayi;
Ngati ulandira Yesu,
Lero, udzachita mwayi.
Lero lino ndi labwino,
Moyo wako uli nawo;
Pena mawa umwalira,
Udzatani mlandu wako?
Lero lino mbale wanga,
Lapa mtima, lapa tchimo;
Yesu adzakulandira,
Ukam’pempha lero lino.
Ndiwe mlendo lero lino,
Myera ndikupempha iwe:
Yesu Mwana wa Mulungu,
Akufuna ndithu iwe.
Inde, lero lino Yesu,
Ayitana inu nonse;
Landirani Mpulumutsi,
Musazengereze konse.
