Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 147 MUSAŴALOLE mawuwo

Chichewa Christian Hymns

Hymn 147 MUSAŴALOLE mawuwo

 

MUSAŴALOLE mawuwo
Apite ngati mphepozi,
Musaumitse mtimatu,
Polira Yesu Mbuyedi.

Idzanitu, idzanitu,
Idzani kwa Ambuyeyo.
Idzanitu, idzanitu
Apulumutse inunso.

Musachitenso nthantha ’yi,
Mufulumire inutu;
Tsiku labwino nleroli,
Mulandirenso moyowu.

Zokondweretsa m’dzikomu
Nzosakhutitsa m’mtimamu,
Koma za Yesu zonsezo
Zikwaniritsa inudi.

Sakukanani Yesudi,
E, mukalapa m’mtimamo;
Lolani kuti Mzimuyo
Agwire ntchito zakezo.

Exit mobile version