Chichewa Christian Hymns
Hymn 143 KONZA mtima iwe mbale,
KONZA mtima iwe mbale,
Pakuleka tchimo;
Siya zonse uzikonda,
Ndikutsata Yesu.
Konza mtima wako lero,
Yesu alowemo;
Ndipo usachedwe iwe,
Taata Yesu lero.
Imva kuyankhula kwake,
Mawu a chikondi;
Ayankhula iwe lero,
Kuti upumule.
Nthawi ya chisomo m’dziko,
Ndi inotu mbale;
Yom’dziwatu Mpulumutsi,
Ukali ndi moyo.
