Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 138 SANGALATSA akusowa, masiku alikutha,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 138 SANGALATSA akusowa, masiku alikutha,

 

SANGALATSA akusowa, masiku alikutha,
Pali anthu otayika, masiku alikutha;
Ngati tikondwerera,
Pakuyenda ulendowu,
Tonse tidzachita bwino, masiku alikutha.

Akutha, akutha, masiku akutha,
Tonse tichitetu bwino, masiku ali kutha.

Tisakhale awulesi, masiku alikutha,
Nkhope zathu zikondwere, masiku alikutha;
Dziko ili ndi lochimwa, lodzaza ndi chisoni,
Thangatani akugwawo, masiku alikutha.

Tamangidwa ndi unyolo, masiku alikutha,
Tisiyetu zoipazi, masiku alikutha;
Tonsefe muzabwinotu
Tidzakhala ndi Mlungu;
Ndipo tidzakondweradi mu nthawi zamuyaya,

Exit mobile version