Chichewa Christian Hymns
Hymn 136 MKAZI wa ku Samariya,
MKAZI wa ku Samariya,
Napita kukatunga madzi;
Pofika iyetu komweko,
Anapeza Ambuye Yesu.
Ambuye ananena:
“Ndipatseni madzi Ndimweko;
Ukanadziwa mtulo wa Mulunguyo,
Sukanandimana madzi.”
Ambuye nanena naye:
“Kayitane mwamuna wako;”
Mkazi anamuyankha nati:
“Inetu ndilibe mwamuna.”
Mkazi pochoka pomwepo,
Natsimikizatu mumtima;
Nati: “Uyu ndiye Mesiya,
Ndi Mwana wa Mulunguyotu.”
Abale tikhulupi’re,
Kuti Ambuye Yesuyo;
Ndiye Mwanadi wa Mulungu,
Ndiponso ndi Mpulumutsiyo.
