Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 135 USANABADWE, Yeremiya,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 135 USANABADWE, Yeremiya,

 

USANABADWE, Yeremiya,
Ine ndinakudziwa;
Ndipo ndinakupatula,
Kuti ukhale mneneri.

Ulalike mawu anga Yeremiya,
Pita ukalalikire
Mawu anga;
Mawu anga Yeremiya.

“Usaopetu nkhope zawo,
Ine ndili ndi iwe;
Kuti ndikulanditsetu,
Iweyo,” ati Yehova.

Usaganize ndiwe mwana,
Iwe udzanka konse;
Kumene ndidzakutuma,
Kuti ukalalikire.

Exit mobile version