Chichewa Christian Hymns
Hymn 13 PAPHIRI ndi padambo,
PAPHIRI ndi padambo,
Ponsepo pali Mlungu;
Poyenda ife m’njira,
MpoYima pali Mlungu.
Kokwera Maganizo,
Komwe kuli Mlungu;
Kumwamba ndi pansipo,
Ponsepo pali Mlungu.
(Mulungu ali nane!)
(Ali nane, ali nane,
ali nane, ali nane, Aa!
Mulungu ali nane!)
Ndi maso Ambuyathu,
Apenyetsetsa ife;
Amadalitsa onse,
Okhulupi’ra Iye.
Amamva timbalame,
Naveka dziko lonse;
Sataya tizirombo,
Asunga zina zonse.
Okwaŵa pansi inu,
Oyenda m’madzi inu;
Oyesa dziko n’kwanu,
A m’mlengalenga inu.
Nonsenu ntchito zake,
Muwona tsiku n’tsiku;
Saleka kusamala,
Ndikudalitsa inu.
Nditama mphamvu yake,
Ya Mlungu yondizinga;
N’kafoka andilimbitsa,
N’kadwala andichiza.
Pakundisiya bwenzi,
Mulungu ali paja;
N’kaloŵa imfa ine,
Alipo Mlungu wanga.
