Chichewa Christian Hymns
Hymn 12 NDITAMATU Ambuyangayu,
NDITAMATU Ambuyangayu,
Moyo wanga wonse ndidzam’tamatu;
Ndiponso m’dziko lakumwambako.
Masiku anga onse ndidzam’lemekeza Iye,
Sindizaleka konsekonse mmene ndili moyotu;
Pa dziko pano pena m’Mwambamo.
Ndiye wokondwa, E, munthuyo,
Wokhulupirira Mlungu yekhadi;
Wolenga dziko, nyanja, zonsezi.
Choona chake chonse chingokhalatu chosatha,
Apulumutsa onse namadyetsa anthu akewo;
Wokonda ndiye Mlungu wathuyo.
Mlungu kuwona athiratu,
Inde m’maso awo osapenyawo;
Natuma akumvera mpumulo.
Amathandiza inde aulendo awo ofokatu,
Akazi amasiye, maka ndi ana’wo onsewo;
Olira otonthoza mtimadi.
Nditama Ambuyangayu,
Moyo wanga wonse ndidzam’tamatu;
Ndiponso m’dziko la Kumwambako.
Masiku anga onse ndidzam’lemekeza Iye,
Sindidzaleka konsekonse mmene ndili moyotu;
Padziko pano pena m’Mwambamo.
