Chichewa Christian Hymns
Hymn 118 PANALI munthu amene,
PANALI munthu amene,
Analimbana ndi mngelo;
Kufikira mbandakucha:
“Sindidzakusiya.”
(M) Ndipo mngelo anati:
(O) “Yakobo iwe, ndisiye;
Kunja kuli kucha, ndisiye,
“Sindidzakusiya!”
Pomwepo mngelo ‘nafunsa:
“Dzina ndi yani?”
“Yakobo,’
“Dzina ndi yani?”
“Yakobo,
Sindidzakusiya.”
Ndipo Mulungu afuna,
Tigwire ntchito yakeyo;
Yolimbana ndi zoipa,
Zodetsa m’mtimamo.
