Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 111 YAKOBO mwanatu wachinyengoyo;

Chichewa Christian Hymns

Hymn 111 YAKOBO mwanatu wachinyengoyo;

 

YAKOBO mwanatu wachinyengoyo;
Wanyenga bambo ake
Kuti, “Inetu ndinetu
Esau mwana wanu.”

Esau analira, “abambo
Inu, abambo anga,
Ndabwera nayo nyama,
Mulandire, mudye.”

Thupi ndi Esau, koma mawuwo,
Ngatitu a Yakobo;
“Bwera mwana wanga,
Bwera pafupi n’kusisite.”

Ndapezatu bwenzi latsopanolo,
Ndi Yesu Mpulumutsi;
Yemwe angathe, kuchotsa,
Machimo anga onse.

Machimo andizunza ine;
Mtima mwangamu inedi,
Ndifuna Inu Mbuye,
Mulowe m’mtima mwanga.

Exit mobile version