Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 106 MZIMU Woyera, mudzetu,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 106 MZIMU Woyera, mudzetu,

 

MZIMU Woyera, mudzetu,
Tiyeretsedwe m’mtimamu;
Mupatse anthu anuwa
Mitulo yanu yonseyo.

Kudzoza kwa Kumwambako
Kutitonthoza m’mtimamo,
Ndi kutidzutsa m’moyomu,
Tikhale okondanatu.

Pankhope pathu mthirepo
Chisomo chanu chijacho;
Mtendere mutininkhebe,
Mutiyendetse ponse phee!

Tionetseni tonsetu
Umodzi wanu wonsemo,
Atate, Mwana, Mzimu ’Nu
Tiimbe Nthaŵi zonsezo:

Titamire Nthaŵi zonse
’Tate, Mwana, Mzimu, Nonse.
Amen

Exit mobile version