Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 105 IDZANI, Mzimu Inu,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 105 IDZANI, Mzimu Inu,

 

IDZANI, Mzimu Inu,
Mundidalitse kuno;
Ndafoka mtima ine
Paulendo wanga uno;
Kwambiri ndakhumudwa
Panjirayo ya moyo;
M’kaleka kutsogola
Ndiwonongeka pompo.

Wakunga mwana ine,
Sindidziŵitsa konse;
Mundilangize Mzimu
Panjira yanga yonse;
Mundiyendetse bwino
Ndifike ine ndemwe
Panjira yolungama,
Kudziko la chimwemwe.

Mundilimbitse m’mtima
Pogwira ntchito izi;
Ndikapumula pena
Mukhale ndithu ndine;
Zolingirira zanga
Ziyere zonse m’mtima
Zoipa muzichotse,
Sindidzazichitanso

Exit mobile version