Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 102 MZIMU Woyera, mudzetu kwa ine

Chichewa Christian Hymns

Hymn 102 MZIMU Woyera, mudzetu kwa ine

 

MZIMU Woyera, mudzetu kwa ine
E, ngati mvula m’dziko lakuuma,
Ndikhale munda wanu wakupatsa
Zipatso zoyenera Mbuyeyo.

Mphunzitsi, ndinu mudziŵitse ine
Chikondi chanu chija chachikulu;
Lembani mawu anu pamtimanga,
Kuti ndikhumbukire zanuzo.

Wosangalatsa, ine ndikalira
Muchotse nsoni, m’mtimamo mudikhe;
Mundigoneke pachifuwa chake
Cha Yesu kuti ndikakondwepo.

Wotsogolera, munditsogolere
Kuti n’kafike kwawo kwa Atate,
Nditsate Yesu ndikuyendayenda
M’njira yomweyo anapondamo.

Mthandizi ndinu, mndithangate ine
Kupempha bwino izo zindisoŵa.
Kupempha monga Mlungu amafuna
Kulingalira zake zokhazo.

Mzimu Woyera, n’dzipereke ndense,
Mundichitire ntchito yaikulu;
Mtima woyera ndi womvera mpatse,
Wodzala ndi chikondi chanucho.

Exit mobile version