Site icon Treasure Hymns – Chichewa

Hymn 100 MUBWERE Mzimu Wakuyera,

Chichewa Christian Hymns

Hymn 100 MUBWERE Mzimu Wakuyera,

 

MUBWERE Mzimu Wakuyera,
Kuyatsa moto m’mtima mwathu;
Ntchito ndi yanu kudzozera
Ndi kutininkha mphatsozo.

Kudzodza kwanu kutipatsa
Chimwemwe, moyo ndi mtendere;
Kuŵala kwanu kupenyetsa
A m’mdima ndi a m’ndendemo.

Mtima wodetsa mukonzere,
Chisomo chanu chakwanira;
Adani athu muthaŵitse

Mutidziŵitse ‘Tate wathu,
Ndi mwana wake ndinu Mmodzi.
Mnafuma kwa aŵiri onse,
Koma Mulungu Mmodziyo

Exit mobile version