Chichewa Christian Hymns
Hymn 90 WINA atikonda ife,
WINA atikonda ife,
Bwenzi lathu ndi ‘Yeyu;
Atifunafuna ife,
Inde, nthawi zonsetu.
Chikondano chakechi,
N’chachikulukuludi.
Ndani mwa abale athu,
Akanatifera’fe?
Koma Yesu m’malo mwathu;
Anapachikidwatu.
Anam’nyoza pansi pano,
Bwenzi la ochimwawo;
Mu ulemelero wake,
Alikonda dzinali.
Tim’chimwira kopambana,
Ndi kumusautsa’Ye;
Koma Bwenzi lathu Yesu,
Atikondakondabe.
M’tiphunzitse, Mbuye Yesu,
Tikondane nanutu;
Tisaiŵalire konse,
Bwenzi lathu Ndinutu.
