Chichewa Christian Hymns
Hymn 72 YESU wakukoma mtima,
YESU wakukoma mtima,
Akondadi!
Wakuposa mbale ndiye,
Akondadi!
Wina asautsa iwe,
Pena adzasiya iwe,
Yesu sadzanyenga iwe,
Akondadi!
Kumdziŵitsa ndiko moyo,
Akondadi!
Akhumbira mtima wako,
Akondadi
Mwazi wake ngwowombola,
M’chipululu akufuna,
M’khola mwake akusunga,
Akondadi!
Akufuna kumdziŵitsa,
Akondadi!
Udzimpatsa moyo wako,
Akondadi!
Kodi umachita mantha?
Pena umadera nkhaŵa?
Yesu amasangalatsa,
Akondadi!
Bwenzi ndiye wakufera,
Akondadi!
Nthaŵi zonse sakusiya,
Akondadi!
Anthu ena akunyenga,
Yesu sadzanyenga iwe,
Zakubvuta adzachotsa,
Akondadi!
Akhululukira iwe,
Akondadi!
Nadzainga mdani wako,
Akondadi!
Adzakudalitsa iwe,
Nadzaletsa tsoka lonse,
Nadzakutsogoza kwawo,
Akondadi!
