Chichewa Christian Hymns
Hymn 59 IMVANI uthenga,
IMVANI uthenga,
Wa imfa ya Yesu;
Wawonadi mavuto,
Mwana wa Mulunguyo.
Tiyeni tipite,
Tikawone Ambuye;
Yesu Mwana wa Mulungu,
Wawonadi mavuto.
Pamtanda Yesuyo,
Anapachikidwa;
Wachotsatu tchimolo,
Kuwombola tonsefe.
Mbale ‘we utani,
Za imfa ya Yesu;
Kodi sumva chisoni,
Tembenuka msangatu.
